Maufulu ndi Maudindo a anthu amene akuchita nawo kafukufuku m'Chichewa

Dokument oor deelnemers se regte en pligte

Mndandanda wa Maufulu ndi Maudindo a anthu amene akuchita nawo kafukufuku unalembedwa koyamba m’Chingelezi m’chaka cha 2003. Mndandandawu unakonzedwanso m’chaka cha 2007 ndipo unamasuliridwa m’ziyankhulo zosiyanasiyana zimene zalembedwa m’munsimu. Mukaganiza zochita nawo Kafukufuku wa Katemera Woyesera wa HIV mudzalandira kabuku ka mafuluwa kolembedwa m’chiyankhulo chimene mungakonde. Mwina kalembedwe ka mawu m’kabuku kamene mungalandire katha kukhala kosiyanako ndi komwe kali m’munsimu.

The Participants' Bill of Rights and Responbilities are available in the following languages:
Afrikaans | BembaEnglish | Nyanja | SepediSetswana | Shona |Sotho | Spanish | Swahili | TsongaXhosa | Zulu | French | Portuguese

Maufulu

Ngati munthu wochita nawo kafukufuku woyeserera Katemera wa HIV muli ndi maufulu awa:

 • Kuwuzidwa bwinobwino zonse zoyenera kuzidziwa pa kafukufukuyu kuphatikizapo zoopsa komanso phindu limene mungapeze pochita nawo kafukufukuyu, Ndipo akufotokozereni moti muthe kumvetsetsa bwinobwino. Mudzauzidwa za mfundo zina zatsopano zimene zingapezeke panthawi ya kafukufukuyu
 • Kukana kulowa nawo mu kafukufukuyu kapena kuchokamo nthawi ina iliyonse. Mutha kukana kulowa nawo mu kafukufuku wina wolondoloza amene angakhalepo mutapemphedwa. Simungalandidwe wina uliwonse mwa maufulu onse amene alembedwa m'chikalata chino pachifukwa chakuti mwakana kapena mwatuluka mu kafukufukuyu.
 • Kuchita kafukufuku mosasankha. Anthu amene akuyendetsa kafukufukuyu adzalemekeza zomwe inu mumakonda, kuziyikira kumtima, zikhulupiriro zanu komanso chikhalidwe chanu.
 • Kupatsidwa mwayi wolandira uphungu komanso chithandizo china chilichonse chokhudzana ndi kafukufukuyu komanso kupewa HIV.
 • Kupatsidwa mwayi wolandira uphungu, chithandizo, mankhwala mukadwala pamene mukuchuita nawo kafukufukuyu kuphatikizapo HIV.
 • Kuthandizidwa pothetsa mavuto ena okhudzana ndi moyo wanu komanso kusalana amene angadze kamba kochita nawo kafukufukuyu. Mutatiloleza tingathe kucheza ndi anthu amene mwatiuza kuti titha kucheza nawo kuti atifotokozere za kuchita nawo kwanu kwa kafukufukuyu.
 • Kulandira chithandizo mukavulala pathupi ngati zitachitika, kuvulala kwina kulikonse kokhudzana ndi zinthu kapena ndondomeko ya kafukufuku yekhayu. Izi zidzachitika motsatira dongosolo limene lalembedwa mu fomu yoperekera chilolezo cholowera mu kafukufukuyu. Tili ndi ndalama za chithandizo cha mankhwala munthu akavulala mukafukufukuyu. Gulu lowona za chitetezo mu kafukufukuyu ndi limene limaunika ndikuvomereza chithandizo cha mankhwala munthu akavulala. Ngati simunakhutire ndi chigamulo cha gululi, chidandaulo chanu chitha kuwunikidwanso. Koma nthawi ndalama sizikhala zokwanira kulipira chithandizo chonse cha mankhwala. Ngati kuli kotheka magulu amene akuyendetsa kafukufukuyu angathe kusaka ndalama zina koma izi sitingalonjeze kuti zidzachitika nthawi zonse. Anthu amene akugwira ntchitoyi m'deralo adzakufotokozewrani za nkhaniyi ndipo adzakuyankhani mafunso alionse amene mungakhale nawo kapena kukulumikizani ndi anthu amene angathe kukuyankhani.
 • Kuyezedwa HIV mwaulere ndi molondola panthawi ya kafukufukuyu. Ngati mutapezeka kuti mwatenga kachirombo ka HIV chifukwa cha katemera wa kafukufukuyu osati njira zina zotengera HIV, mutha kuyezedwanso kena pachipatala cha kafukufukuyo mpaka mutapezeka wopanda HIV.
 • Kuthandizidwa pokwaniritsa zoyenera kuchita pa kafukufukuyu. Anthu ogwira ntchito ya kafukufukuyu adzakupatsani mndandanda wa zinthu zimene mungalandire kapena kugwiritsa ntchito pakafukfukuyu.
 • Kusunga chinsinsi. Zokambirana komanso zolembalemba zokhudzana ndi inuyo komanso kuchita nawo kwanu kwa kafukufukuyu zidzaperekedwa kwa anthu ena pazifukwa zokhazo zokhudzana ndi kuchitika kwa kafukufukuyu kapena movomerezedwa ndi malamulo. Kuti mumve zambiri werenganni fomu yoperekera chilolezo chichitira nawo kafukufukuyu.
 • Mupatsidwe khadi ya chizindikiro chosonyeza kuti mukuchita nawo kafukufukuyu. Khadili lomwe mutha kusankha kukhala nalo kapena ayi lidzalembedwa nambala yanu ya foni, keyala yanu kapena munthu amene angafotokoze zina za inu.
 • Kupitiriza kukhala ndi ufulu wachilamulo. Pamene mukuchita nawo kafukufukuyu, sindiye kuti mukuthetsa maufulu anu.
 • Muwuzidwe ngati mwalandira mankhwala ongonamizira (placebo) kapena katemera kafukufukuyu akatha, kapena pamene achipatala aona kuti ndikofunikira kutero.
 • Kudziwitsidwa za momwe kafukufuku akuyendera, kuwuzidwa zotsatira nthawi imene zotsatira zidzatulukire ndi momwe mungadziwire za zotsatirazo.

Maudindo

Ngati wochita nawo kafukufuku woyeserera katemera wa HIV, muli ndi udindo wochita izi:

 • Kuwunika ndi kusonyeza kumvetsa zipangizo zonse zimene mwapatsidwa kuphatikizapo fomu yoperekera chilolezo chochita nawo kafukufukuyu. Funsani kuti akufotokozereni za china chilichonse chomwe simukumvetsetsa musanavomere kuchita nawo kafukufukuyu. Mungathenso kufunsa mafunso panthawi ina iliyonse ya kafukufukuyu.
 • Ganizirani mofatsa polowa nawo m'kafukufukuyu mutaunika kuopsa kwake komanso phindu lake. Muyenera kumvetsetsa zonse zokhudza kafukufukuyu. Akuluakulu ogwira ntchito ya kafukufukuyu adzakuthandizani. Muthanso kukambirana ndi anthu amene mumawadalira kuti akuthandizeni maganizo ngati kuli koyenera kulowa nawo m'kafukufukuyu.
 • Fotokozerani mwachangu ogwira ntchito ya kafukufukuyu ngati mwaona kuti mukusalidwa kapena mukukumana ndi vuto lina lake pamoyo wanu chifukwa chakuti mukuchita nawo kafukufukuyu.
 • Pamene mukuchita nawo kafukufukuyu musapereke magazi kapena ziwalo kapenanso madzi ena alionse a m'thupi.
 • Muyenera kuyezetsa HIV pamalo pamene pakuchitikira kafukufukuyu pa nthawi ina iliyonse ya kafukufukuyu. Kambiranani ndi anthu ogwira ntchito ya kafukufukuyu ngati mukufuna kukayezedwa kwina
 • Ingati muli oti mutha kutenga pakati, muyesetse kusatenga pakati panthawi ya kafukufukuyu pogwiritsa ntchito njira zolelera. Akuluakulu ogwira ntchito ya kafukufukuyu adzakuthandizani kuwunika njira zabwino zolelera.
 • Muyenera kupita kuchipatala nthawi zonse zimene munauzidwa. Dziwitsani akuluakulu akafukufukuyu ngati mukufuna kusintha tsiku lopitira kuchipatala
 • Perekani ulemu kwa anthu ogwira ntchito ya kafukufuku.
 • Sungani chinsinsi pa za anthu ena amene akuchita nawo kafukufukuyu.
 • Muwauze anthu amene akuchita nawo kafukufukuyu zoona zonse zokhudzana ndi kafukufuku. Ngati pali kusintha pa keyala kapena za umoyo wanu adziwitseni amene akugwira ntchito ya kafukufukuyu
 • Yesetsani kutsatira malangizo amene mwapatsidwa ndi akuluakulu a kafukufukuyu. Gwirani ntchito limodzi ndi anthu ena ogwira ntchito za kafukufukuyu kuti mukhale otetezeka panthawi yonse ya kafukufukuyu
 • Dziwitsani akuluakulu ogwira ntchito ya kafukufukuyu ngati simukwanitsa kupitiriza kuchita nawo kapena mwaganiza zosiya kuchita nawo kafukufukuyu.