Mndandanda Wa Maufulu Ndi Maudindo (Bill of Rights and Responsibilities, BRR) Pa Kafukufuku Wa HIV
Chikalata chino chikufotokoza mndandanda waufupi wa maufulu ndi maudindo amene muli nawo pamene mukutenga nawo mbali mu kafukufuku wa HIV. Cholinga cha mndandandawu ndi kuthandiza anthu amene akutenga nawo mbali mu kafukufukuyu kuti azichita zinthu mwa iwo okha komanso pamodzi ndi gulu la anthu ochita kafukufuku. Kuti mudziwe zambiri werengani fomu yofotokoza za chilolezo chochitira nawo kafukufukuyu.
Ufulu Wa Anthu Otenga Nawo Mbali Mu Kafukufuku
Ngati wotenga nawo mbali mu kafukufuku wa HIV/Edzi yemwe akuchititsa ndi a HVTN muli ndi ufulu wochita izi:
- Kukhala ndi uthenga wonse womwe ukudziwika pa za kafukufukuyu kuphatikizapo kuopsa ndi ubwino wochita nawo kafukufukuyu ndipo uthengawo uyenera kuperekedwa kwa inu momveka bwino. Mudzauzidwa za uthenga wina watsopano umene ungadziwike pa nthawi yomwe kafukufukuyu ali m’kati.
- Mafunso anu onse ayankhidwe.
- Kukana kulowa mu kafukufukuyu kapena kusiyira panjira nthawi ina iliyonse. Muthanso kukana kuchita nawo kafukufuku wina wotsatira amene mwapemphedwa. Simudzataya ufulu wanu umene taufotokoza muchikalata chino chifukwa chakuti mwakana kutenga nawo mbali kapena kusiyira panira kafukufukuyu.
- Kusasalidwa pamene mukuchita nawo kafukufuku. Ogwira ntchito ya kafukufuku adzalemekeza zisankho za moyo wanu, zinthu zimene mumaziyikira kumtima, zikhulupiriro zanu komanso chikhalidwe chanu.
- Kutumizidwa kwina kuti mukalandire uphungu, chithandizo cha mankhwala pa matenda amene mwadwala pamene mukutenga nawo mbali mu kafukufukuyu kuphatikizako HIV.
- Kuthandizidwa pothana ndi mavuto okhudza moyo wanu amene angadze kamba ka kafukufukuyu komanso kusalidwa. Mutatipatsa chilolezo titha kukambirana ndi anthu amene mungatiuze kuti tiwafotokozere zambiri zokhudza kutenga nawo kwanu mbali mu kafukufukuyu.
- Kulandira chithandizo cha mankhwala mutavulala, kapena pa vuto lina lililonse lodza kamba ka mankhwala kapena zochitika mu kafukufukuyu mogwirizana ndi momwe tafotokozera mu fomu yoperekeera chilolezo chochitira nawo kafukufukuyu. Pali ndalama zothandizira kulipilira chithandizo cha mankhwala ngati mwavulala kapena kudwala. Pali gulu limene limaunika ngati kuvulala kwanu kukukhudzana ndi kafukufuku. Ngati simukugwirizana ndi chigamulo chawo mutha kupempha kuti nkhani yanu ayiunikenso. Nthawi zina, ndalama zimakhala zosakwanira kulipira chithandizo chonse cha mankhwala. Magulu amene akuchititsa kafukufukuyu adzafufuza ndalama zina zowonjezera ngati kuli kofunika kutero, koma sikuti nthawi zonse zimatheka kupeza ndalamazo. Ogwira ntchito ya kafukufuku adzakufotokozerani zambiri za nkhaniyi ndipo adzakuyankhani mafunso ena alionse amene mungakhale nawo kapena kukulumikizani ndi munthu amene angathe kuyankha bwino mafunso anu.
- Kuyezetsa HIV mwaulele komanso zotsatira zake zolondola pamene mukutenga nawo mbali mu kafukufukuyu. Ngati pakutha pa kafukufukuyu, zotsatira za kuyezetsa kwanu zikusonyeza kuti muli ndi HIV chifukwa cha mankhwala kapena zipangizo zina zomwe munalandira mu kafukufukuyu, koma osati kuti muli ndi kachirombo ka HIV, mutha kuyezedwanso kuchipatala cha kafukufukuyu kapena kudzera mu HVTN mpaka zotsatirazo zitasonyeza kuti mulibe HIV.
- Kuthandizidwa kuti mukwaniritse zofunikira mu kafukufukuyu. Ogwira ntchito pachipatala cha kafukufuku adzakupatsani mndandanda wa zinthu zimene muyenera kukhala nazo.
- Kusunga chinsinsi. Mauthenga onse komanso mbiri yanu ndi kutenga nawo mbali kwanu mu kafukufukuyu zidzaperekedwa kwa anthu ena pokhapo pamene kuli kofunikira poyendetsa kafukufukuyu kapena pamene kuli kofunikira ndi lamulo. Werengani fomu yoperekera chilolezo chochitira nawo kafukufuku kuti mudziwe zambiri.
- Kupatsidwa chiphaso cha chizindkiro chosonyeza kuti mukutenga nawo mbali mu kafukufukuyu. Pachiphasochi padzakhala nambala ya foni ndi keyala ya munthu amene angafotokoze zambiri za kafukufukuyu.
- Kupitiriza kukhala ndi ufulu wachilamulo. Angati munthu wotenga nawo mbali mu kafukufuku, sikumutaya ufulu wanu wina uliwonse.
- Kuuzidwa ngati mwalandira katemera wopanda mankhwala kapena katemera weniweni kafukufukuyu akatha kapena pamene kuli kofunikira kukukuzani malinga ndi ndondomeko ya za umoyo.
- Kuuzidwa pafupipafupi momwe kafukufukuyu akuyendera, kuuzidwa nthawi imene zotsatira zidzatuluke ndikuti ogwiria ntchito ya kafukufuku akufotokozereni zotsatira za kafukufuku.
- Kudziwa ngati pali ndalama zimene muyenera kugwiritsa ntchito pochita nawo kafukufukuyu komanso ngati mudzalandira chipukutamisozi chifukwa chotenga nawo mbali mu kafukufukuyu.
Udindo wa Otenga Nawo Mbali mu Kafukufuku
Inu monga otenga nawo mbali mu kafukufuku wa HVTN wofufuza za HIV ndi Edzi muli ndi udindo uwu:
- Kuzukuta ndi kuonetsa kuti mukumvetsetsa uthenga wa mu zikalata zonse zimene mwapatsidwa kuphatikizapo fomu yoperekera chilolezo chochitira nawo kafukufuku. Funsani kuti akufotokozereni chilichonse chomwe simukumvetsa musanavomere kutenga nawo mbali mu kafukufukuyu. Muthanso kufunsa mafunso nthawi ina iliyonse kafukufukuyu ali m’kati.
- Pangani chiganizo mozindikira chomwe mukuchita ngati mukufuna kutenga nawo mbali mu kafukufukuyu kapena ayi mutayamba mwaganizira koopsa komanso ubwino wake wochita nawo kafukufukuyu. Ndikofunikira kudziwa zomwe zikuchitika mu kafukufukuyu. Ogwira ntchito ya kafukufukuyu adzakuthandizani kukufotokozerani zambiri zokhudza kafukufukuyu. Ngati mukuganiza kuti zingakuthandizeni kupanga chiganizo chotenga nawo mbali mu kafukufukuyu, kambiranani ndi anthu amene mumawakhulupirira ndi kuwadalira kuti akulangizeni ngati kuli koyenera kuti mutenge nawo mbali mu kafukufukuyu.
- Dziwitsani mwachangu ogwira ntchito ya kafukufuku ngati mukuona kuti mwasalidwa kapena mwakumana ndi vuto lina pa moyo wanu lomwe mukuganiza kuti ladza kamba ka kutenga nawo mbali kwanu mu kafukufukuyu.
- Musapereke kwa munthu wina magazi kapena ziwalo kapena madzi ena a m’thupi pa nthawi imene mukutenga nawo mbali mu kafukufukuyu.
- Yezetsani HIV pachipatala cha kafukufukuyu chokha basi pa nthawi yonse yomwe mukutenganga nawo mbali mu kafukufukuyu. Kambiranani ndi ogwira ntchito ya kafukufukuyu ngati mukufuna kukayezetsa kwina.
- Ngati muli akuti mutha kutenga pakati, pewani kutenga pakati pa nthawi yomwe mukuchita nawo kafukufukuyu pogwiritsa ntchito njira za kulera zolula. Ogwira ntchito ya kafukufukuyu adzakuthandizani kusankha njira yolerera yokuyenerani.
- Kwaniritsani masiku anu opita kuchipatala cha kafukufuku. Dziwitsani ogwira ntchito ya kafukufuku mwachangu ngati mukufuna kusintha tsiku lopitira kuchipatala.
- Perekani ulemu kwa ogwira ntchito ya kafukufuku.
- Sungani mwachinsinsi nkhani za anthu ena amene akutenga nawonso mbali mu kafukufukuyu.
- Auzeni zolondola komanso zokwanira ogwira ntchito ya kafukufuku. Auzeni ogwira ntchito ya kafukufuku ngati foni kapena keyala yanu komanso ngati umoyo wanu wasintha.
- Yesetsani momwe mungathere kutsatira malangizo ochokera kwa ogwira ntchito ya kafukufuku. Gwirani limodzi ntchito ndi anthu a kafukufuku kuti moyo wanu ukhale wotetezedwa nthawi yonse yomwe mukutenga nawo mbali mu kafukufuku.
- Ngati simungathe kupitiriza kapena mwaganiza zotuluka mu kafukufuku, dziwitsani mwachangu ogwira ntchito ya kafukufuku.
Udindo Wa Ogwira Ntchito Ya Kafukufuku
Ogwira ntchito ya HVTN, kuphatikizapo Mkulu wa Kafukufuku pachipatala pano ali ndi udindo wochita izi:
- Kukambirana ndi anthu am’derali pa nkhani zokhudza kafukufukuyu ndi kuonetsetsa kuti pali chiwerengero choyenera cha anthu a m’derali amene akutenga nawo mbali mu kafukufukuyo.
- Tumikirani ndi kutsatira malangizo ochokera ku bungwe loyang’anira kafukufuku monga bungwe lowunika momwe kafukufuku akuyenera kuyendera la Institutional Review Board (IRB) kapena mabungwe ena a owona ngati kafukufuku akuchitika motsata ndondomeko.
- Kupeza chilolezo chochitira nawo kafukufuku kwa anthu amene akutenga nawo mbali mu kafukufuku. Ngati pali kusintha kwakukulu pa kafukufuku ndikofunika kutenga chilolezo china chochitira nawo kafukufuku
- Chitani kafukufuku mwandondomeko, kuphatikizapo kuteteza ufulu komanso kusunga chinsinsi cha anthu amene akutenga nawo mbali mu kafukufukuyo. Pakutha pa kafukufuku, ogwira ntchito ya kafukufuku ali ndi udindo wodziwitsa anthu amene amatenga nawo mbali za mankhwala amene anali kulandra mu kafukufukumo komanso kuwafotokozera anthu ndi ena onse am’deralo zotsatira za kafukufukuyu.
- Kutumiza anthu ochita nawo kafukufuku kuchipatala kwina kuti akalandire uphungu, chithandizo choteteza HIV, chithandizo cha mankwhala a HIV ndi/kapena uphungu wokhudza umoyo wa maganizo.
- Kuyankha mwachangu mafunso komanso madandaulo onse amene otenga nawo mbali mu kafukufuku ali nawo
- Perekani ulemu kwa otenga nawo mbali mu kafukufuku.