Mndandanda Wa Maufulu Ndi Zofunikila Kuchita (Bill of Rights and Responsibilities, BRR) Mu Kafukufuku Wa HIV

Iyi pepala ipasa mndandanda wa maufulu and zomwe mufunikila kuchita pamene mutengako mbali mu kafukufuku wa HIV wamene kiliniki ichita moyesa yomwe muchizungu akuti HIV Vaccine Trials Network (HVTN) clinical trial. Cholinga cha mndandanda wa maufulu ndi zinchito ndikuthandiza otengako mbali mu kafukufuku kuti azichitile zinthu komanso kuchita moimilila oyendesa kafukufuku. Onani pepala yamene ili nawo uthenga wachiziwiso kwa otengako mbali mu kafukufuku kuti muziwe zambiri.

The Participants' Bill of Rights and Responbilities are available in the following languages:

Maufulu a Otengako Mbali

Monga otengako mbali mu kafukufuku wa HVTN HIV/AIDS, muli nawo ufulu wa:

  • Kukhala nawo uthenga onse wofunikila kuziwa, kuikapo ziopsyezo ndi mapindu otengako mbali mu kafukufuku mu njila yamene mungathe kumvesesa. Muzaziwisidwa za uthenga uli onse wasopano mukuyenda mwa kafukufuku.
  • Mafunso anu onse kuyankhidwa. 
  • Kukana kulowa olo kuchoka mu kafukufuku pa nthawi ili yonse. Mungakanenso makafukufuku amene asatila pambuyo pake yamene muzauzidwa. Simuzataya maufulu alionse amene achulidwa mu pepala iyi ngati mwakana kulowa kapena kuchoka mu kafukufuku.
  • Ulemu mu malo yamene muzachitila kafukufuku. Kusankha kwanu, mwambo, zikhulupililo ndi maganizo anu azalemekezedwa ndi anthu oyendesa kafukufuku.
  • Kukupelekani ku uphungu, thandizo, mankhwala ndi chiliso ya matenda yamene mungayambile pamene muli kutengako mbali mu kafukufuku, kuikapo HIV.
  • Thandizo yothesa mavuto a umunthu amene mungapeze. Kupyolela mu chilolezo chanu, tingakambe ndi anthu amene mungatiuze kuti tikambe nawo kuwamasulila bwino za kutengako mbali kwanu mu kafukufuku uyu.
  • Mankhwala a kupwetekedwa kwa thupi, ngati kwachitika, ndi kupwetekedwa kuli konse kwamene kwabwela chifukwa cha mankhwala kapena ndondomeko za mu kafukufuku uyu kulingana ndi uthenga uli mu pepala ya kuvomela kwanu kutengako mbali moziwisidwa. Kuli ndalama zolipila ku kupwetekedwa uku. Bungwe yamene iyang’ana pa kukhala kwanu mu kafukufuku imaona ngati vuto yabwela chifukwa chotengako mbali mu kafukufuku. Mungafunse kuti kulamula kwawo kusinthidwe ngati simuvomela nako kulamulila kwao. Nthawi zina, ndalama sizingankhale zokwana kupasa mankhwala onse. Magulu oyanjana ndi kafukufuku angasakile ndalama ngati zifunika koma sangalonjeze kuti zonse zizatheka. Oyendesa kafukufuku uyu azakupasani uthenga wambiri ndipo azayankha mafunso yamene muli nayo olo kukuthandizani kuona munthu wamene angakhale oziwa bwino kuyankha mafunso yanu.
  • Chipimo cha ulele komanso choona cha kalombo ka HIV. Ngati, pothela pa kafukufuku zioneka ngati muli ndi HIV, y chifukwa za zosewenzesa mu kafukufuku osati kuti muli nayo, mungalandile zipimo zaulele pa kiliniki kupyolela mu chipimo cha a HVTN’ mpaka mwapezeka kuti mulibe HIV.
  • Thandizo yoti mukwanise zofunikila kuchita mu kafukufuku. Mndandanda wa zinthu zomwe ziliko zizapasidwa kwa inu ndi dela yamene iyendesa kafukufuku wanu. 
  • Chisinsi. Kukambisana ndi uthenga wanu ndi kutengako mbali kwanu mu kafukufuku uzapasidwa chabe mukuyendesa kafukufuku olo ngati wafunika kulingana ndi lamulo. Onani pepela ya kutengako mbali mu kafukufuku kwanu moziwisidwa kuti muziwe zambiri.
  • Kukupasani chitupa choonesa kuti muli kutengako mbali mu kafukufuku. Ichi chitupa kapena kuti khadi izakhala nayo nambala ya foni ndi keyala ya munthu wamene angakupaseni uthenga wowonjezelapo.
  • Kukhala nawo maufulu a lamulo. Ngati otengako mbali mu kafukufuku woyesa, simutaya ufulu wanu uli onse.
  • Kuuziwa ngati munalandilapo placebo kapena chosenzesa china chili chose mu kafukufuku pothela pa kafukufuku, olo kapena kulingana ndi kufunika kwa zamankhwala.
  • Kuuziwa za mwamene kafukufuku ayendela, kuuziwa pamane zotulukamo mu chipimo chanu zakhalako ndi anthu oyendesa phunzilo kukupasani ndi kugawana ndi inu zotulukamo mu zipimo.
  • Kuziwa ngati mufunika kulipila kuti mutengeko mbali mu kafukufuku olo kapena kuti muzapasidwa ndalama chifukwa chotengako mbali mu phunzilo.

Zintchito za otengako mbali mu Kafukufuku

Ngati otengako mbali mu kafukufuku woyanjana ndi HVTN HIV/AIDS, muli nayo ntchito ya:

  • Kupitamo ndi kuonesa kuti mwamvesesa zinthu zonse zomwe mwapasidwa kuikapo pepala ya chivomekezo chanu kutengako mbali mu kafukufuku. Kufunsa funso iliyonse ya uthenga wamene simumvesesa mukalibe kuvomela kuengako mbali mu kafukufuku. Mungafunsenso nthawi iliyonse mukati mwa kafukufuku.
  • Kupanga ganizo kuti ngati mufuna kutengako mbali mu kafukufuku kapena iyayi pambuyo pakuona ziopsyezo komanso mapindu. Nichofunikila kuziwa cholinga cha kafukufuku. Anthu oyendesa kafukufuku azakuthandizani pali izi. Ngati chizakuthandizani kupanga ganizo, kambani ndi anthu amene muwakhulupilila ndi kupasa ulemu kuti akuthandizeni kupanga ganizo kuti ngati kutengako mbali mu kafukufuku kukuyenelani kapena iyayi.
  • Uzani oyendesa kafukufuku mwamsanga ngati mupeza vuto iliyonse yamene yabwela chifukwa chotengako mbali mu kafukufuku.
  • Osapasa magazi, kapena ziwalo kapena manzi alionse kufuma muthupi pamene muli kutengako mbali mu kafukufuku.
  • Muzipimisa HIV pa kiliniki yanu ya kafukufuku pa nthawi yonse yamene muli kutengako mbali mu kafukufuku. Kambani nawo oyendesa kafukufuku ngati mufuna kukapimisila kwina kwake.
  • Ngati mukwanisa kutenga mimba, pewani kutenga mimba pamene mutengako mbali mu kafukufuku kupyelera kusewenzesa njila zopewelamo mimba. Anthu oyendesa kafukufuku azakuuzani njila zabwino zomwe mungapewelemo kutenga mimba.
  • Bwelani ku kumana kwa mukafukufuku mosalephela. Aziwiseni oyendesa kafukufuku mwamsanga ngati simuzakwanisa kubwela kuti muike siku ina yoti mukabwele.
  • Pasani ulemu anthu amene ayendesa kafukufuku.
  • Sungani chisinsi cholingana ndi kutengako mbali mu kafukufuku kwa anthu ena.
  • Pasani anthu oyendesa kafukufuku uthenga wokwana komanso wazoona woyanjana ndi kafukufuku. Aziwiseni anthu oyendesa kafukufuku ngati mwasintha zili zonse pa uthenga wanu ndi za thanzi yanu.
  • Satilani malangizo omwe oyendesa kafukufuku akupasani mokwana ndithu. Sewenzani pamozi ndi oyendesa kafukufuku kuti musunge thanzi lanu bwino pa nthawi ya kafukufuku.
  • Aziwiseni mwamsanga anthu oyendesa kafukufuku ngati simuzakwanisa kupitiliza olo kapena mwaganiza kuleka kutengako mbali mu kafukufuku.

Zinchito za anthu oyendesa Kafukufuku

Anthu oyendesa kafukufuku wa HVTN, kuikapo ndi mkulu wa kafukufuku (PI) pa kiliniki pano, ali ndi zinchito za:

  • Kufunsa anthu a m’mudzi pa zinthu zoyanjana ndi kafukufuku ndi kuona kuti anthu onse a m’magulu osiyanasiyana atengako mbali mu kafukufuku wa pa kiliniki.
  • Kuyankha mafunso komanso kulandila malamulo kuchokela ku bungwe yomwe iyendesa kafukufuku uyu monga bungwe ya Institutional Review Board (IRB) olo mabungwe ofanana nawo oyendesa malamulo a moyendesela kafukufuku.
  • Kutenga chivomekezo kuchoka kwa onse otengako mbali mu kafukufuku mu mbali zonse zokhuza kafukufuku. Ngati kuli zikulu zizasinthika, azatenganso chivomekezo china.
  • Kuchita kafukufuku mosatila lamulo, kuikapo kuteteza maufulu, chinsinsi ndi mnkhalidwe wa bwino wa anthu omwe ali mu kafukufuku. Pothela pa kafukufuku, oyendesa kafukufuku ali nayo nchito yokuziwisani zinthu zomwe anali kulandila ndi kukupasani zotulukamo mu kafukufuku komanso a m’mudzi. 
  • Kupeleka anthu komwe angalandile uphungu, kuthandiza anthu momwe angapewele HIV, kupasa mankhwala ya HIV ndi thandizo ya zokhuza maganizo ndi umunthu pamene munthu atenga mbali mu kafukufuku. 
  • Kuyankha mafunso ndi zofunikila zina za otengako mbali mu kafukufuku pa nthawi yabwino.
  • Kupasa ulemu anthu otengako mbali mu kafukufuku.